-
1 Mafumu 7:38, 39Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
38 Kenako anapanga mabeseni 10 akopa.+ Mʼbeseni lililonse munkalowa madzi okwana mitsuko 40, ndipo linali mikono 4 kuchokera mbali ina kufika mbali ina. Pa zotengera 10 zija, chilichonse chinali ndi beseni lake. 39 Anaika zotengera 5 mbali yakumanja kwa nyumbayo komanso zotengera 5 mbali yakumanzere. Thanki ija anaiika kumanja kwa nyumbayo, kumʼmwera chakumʼmawa.+
-