-
2 Mbiri 28:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Ndipo pa nthawi imene Mfumu Ahazi ankakumana ndi mavuto, anawonjezera kuchita zosakhulupirika kwa Yehova. 23 Ahaziyo anayamba kupereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko+ imene inamugonjetsa,+ ndipo anati: “Milungu ya mafumu a Siriya ikuwathandiza, choncho ndipereka nsembe kwa milunguyi kuti inenso indithandize.”+ Koma milunguyo inachititsa kuti iye ndi Aisiraeli onse akumane ndi mavuto.
-
-
Yeremiya 44:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 “Nsembe zimene inuyo, makolo anu, mafumu anu, akalonga anu ndi anthu amʼdzikolo ankapereka mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu,+ Yehova anazikumbukira ndipo zinalowa mumtima mwake.
-