-
2 Mbiri 15:10-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Iwo anasonkhana ku Yerusalemu mʼmwezi wachitatu wa chaka cha 15 cha ulamuliro wa Asa. 11 Pa tsiku limeneli, anapereka nsembe kwa Yehova kuchokera pa zinthu zimene anatenga kwa adani awo. Anapereka nsembe ngʼombe 700 ndi nkhosa 7,000. 12 Kuwonjezera pamenepo, anachita pangano loti adzafunafuna Yehova Mulungu wa makolo awo ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse.+ 13 Komanso kuti aliyense wosafunafuna Yehova Mulungu wa Isiraeli ayenera kuphedwa, kaya ndi wamngʼono kapena wamkulu, mwamuna kapena mkazi.+
-