Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • Levitiko 4:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ngati wansembe wodzozedwa+ wachita tchimo+ ndipo lapangitsa anthu onse kupalamula, azipereka kwa Yehova ngʼombe yaingʼono yamphongo yopanda chilema monga nsembe yamachimo chifukwa cha tchimo lakelo.+

  • Levitiko 4:13, 14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Tsopano ngati gulu lonse la Isiraeli lapalamula pochita tchimo mosadziwa,+ koma mpingo* sunazindikire kuti iwo achita zimene Yehova anawalamula kuti asachite,+ 14 ndipo kenako tchimolo ladziwika, mpingowo uzipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo, ndipo azibwera nayo pakhomo la chihema chokumanako.

  • Numeri 15:22-24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Koma mukalakwitsa zinthu nʼkulephera kusunga malamulo onsewa amene Yehova walankhula kudzera mwa Mose, 23 zonse zimene Yehova wakulamulani kudzera mwa Mose, kuchokera pa tsiku limene Yehova analamula mpaka mʼtsogolo mʼmibadwo yanu yonse, 24 ngati mwalakwitsa mosazindikira, ndipo gulu lonselo silinadziwe, gulu lonselo lizikapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzikapereka nsembeyo limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ Muzikaperekanso mbuzi yaingʼono imodzi kuti ikhale nsembe yamachimo.+

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani