-
1 Mbiri 28:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Anamupatsanso mapulani a kamangidwe ka zonse zimene anauzidwa kudzera mwa mzimu zokhudza mabwalo+ a nyumba ya Yehova, zipinda zonse zodyera kuzungulira kachisi, mosungira chuma cha nyumba ya Mulungu woona ndi mosungira zinthu zimene anaziyeretsa kuti zikhale zopatulika.+ 13 Komanso anamʼpatsa malangizo okhudza magulu a ansembe+ ndi a Alevi, ntchito yonse yokhudza utumiki wapanyumba ya Yehova ndiponso malangizo okhudza ziwiya zonse za utumiki wapanyumba ya Yehova.
-