-
1 Mbiri 29:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Anthuwo anayamba kupereka nsembe kwa Yehova ndipo anapereka nsembe zopsereza+ kwa Yehova mpaka tsiku lotsatira. Anapereka ngʼombe zamphongo zazingʼono 1,000, nkhosa zamphongo 1,000, ana a nkhosa amphongo 1,000 ndi nsembe zake zachakumwa.+ Iwo anapereka nsembe zambirimbiri za Aisiraeli onse.+ 22 Pa tsikulo, iwo anadya ndi kumwa mosangalala kwambiri+ pamaso pa Yehova. Kachiwirinso, anaveka Solomo mwana wa Davide ufumu ndipo anamudzoza pamaso pa Yehova kukhala mtsogoleri.+ Anadzozanso Zadoki kukhala wansembe.+
-