2 Koma mfumuyo, akalonga ake ndi gulu lonse la anthu ku Yerusalemu anagwirizana zoti achite Pasikayo mwezi wachiwiri.+ 3 Iwo sanathe kuchita Pasikayo pa nthawi imene ankayenera kuchita+ chifukwa ansembe amene anadziyeretsa+ anali osakwanira komanso anthu anali asanasonkhane ku Yerusalemu.