-
Numeri 12:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Yehova anauza Mose kuti: “Kodi bambo ake akanamulavulira malovu kumaso, sakanakhala wonyozeka kwa masiku 7? Ndiye mʼtulutseni akakhale kunja kwa msasa+ kwa masiku 7, pambuyo pake mumulowetsenso mumsasamo.”
-
-
Deuteronomo 25:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 mkazi wamasiyeyo aziyandikira mchimwene wa mwamuna wakeyo akuluwo akuona ndipo azimuvula nsapato+ nʼkumulavulira kumaso nʼkunena kuti, ‘Izi nʼzimene ziyenera kuchitikira munthu amene wakana kumanga nyumba ya mchimwene wake.’
-
-
Yesaya 50:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Msana wanga ndinaupereka kwa anthu amene ankandimenya
Ndipo masaya anga ndinawapereka kwa anthu amene ankandizula ndevu.
Sindinabise nkhope yanga kuti asaichitire zinthu zochititsa manyazi komanso kuti asailavulire.+
-