114 Isiraeli atatuluka mu Iguputo,+
Nyumba ya Yakobo itatuluka pakati pa anthu olankhula chilankhulo chachilendo,
2 Yuda anakhala malo ake opatulika,
Ndipo Isiraeli linakhala dziko limene ankalilamulira.+
3 Nyanja inaona zimenezi ndipo inathawa,+
Yorodano anabwerera mʼmbuyo.+