-
2 Mbiri 36:17-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Choncho anawabweretsera mfumu ya Akasidi+ yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga+ mʼnyumba yopatulika.+ Sinamvere chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena wodwala.+ Mulungu anapereka zonse mʼmanja mwake.+ 18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse, zazikulu ndi zazingʼono, zamʼnyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma cha mʼnyumba ya Yehova, chuma cha mfumu ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse nʼkupita nacho ku Babulo.+ 19 Inatentha nyumba ya Mulungu woona,+ kugwetsa mpanda wa Yerusalemu,+ kutentha nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndiponso zinthu zonse zamtengo wapatali.+
-
-
Yeremiya 52:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu, nyumba iliyonse yaikulu komanso nyumba zonse za mu Yerusalemu.
-