22 Ine ndidzamuweruza pomubweretsera mliri+ ndipo anthu ambiri adzafa. Ndidzamugwetsera mvula yamphamvu, matalala,+ moto+ ndi sulufule.+ Ndidzagwetsa zinthu zimenezi pa iyeyo, magulu a asilikali ake ndi mitundu yambiri ya anthu amene adzakhale kumbali yake.+