17 Pakati pa khonde ndi guwa la nsembe,+
Ansembe omwe ndi atumiki a Yehova alire nʼkumanena kuti:
‘Inu Yehova, mverani chisoni anthu anu,
Ndipo musachititse manyazi cholowa chanu,
Kuti anthu a mitundu ina awalamulire.
Anthu a mitundu ina asanene kuti: “Kodi Mulungu wawo ali kuti?”’+