-
1 Samueli 2:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Musamalankhule modzikweza,
Pakamwa panu pasatuluke mawu odzikuza,
Chifukwa Yehova ndi Mulungu wodziwa zonse,+
Ndipo zochita za anthu, iye amaziyeza molondola.
-
-
Ezekieli 28:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Iwe mwana wa munthu, uza mtsogoleri wa Turo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Chifukwa chakuti wadzikuza mumtima mwako,+ ukumanena kuti, ‘Ndine mulungu.
Ndakhala pampando wachifumu wa mulungu pakatikati pa nyanja.’+
Koma ndiwe munthu basi, osati mulungu,
Ngakhale kuti mumtima mwako umadziona kuti ndiwe mulungu.
-