3 Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.+
Zimenezi zinditsogolere.+
Zinditsogolere kuphiri lanu lopatulika ndi kuchihema chanu chachikulu.+
4 Kenako ndidzapita paguwa lansembe la Mulungu,+
Kwa Mulungu amene amandisangalatsa kwambiri.
Ndipo ndidzakutamandani ndi zeze+ inu Mulungu, Mulungu wanga.