6 Mʼphiri ili,+ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzakonzera anthu a mitundu yonse,
Phwando la zakudya zabwino kwambiri,+
Phwando la vinyo wabwino kwambiri,
Phwando la zakudya zabwinozabwino zokhala ndi mafuta amʼmafupa,
Ndiponso la vinyo wabwino kwambiri, wosefedwa bwino.