-
Danieli 9:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Ndili mkati molankhula, kupemphera ndi kuvomereza machimo anga ndi machimo a anthu a mtundu wanga, Aisiraeli komanso kupempha Yehova Mulungu wanga kuti andikomere mtima pa nkhani yokhudza phiri loyera la Mulungu wanga,+ 21 inde, ndili mkati molankhula zimenezi mʼpemphero, munthu uja Gabirieli,+ amene ndinamuona mʼmasomphenya poyamba paja,+ anabwera kwa ine nditatopa kwambiri, pa nthawi yopereka nsembe yamadzulo imene imaperekedwa ngati mphatso.
-