19 Pamene ankanena zimenezi nʼkuti inu mulipo ochepa,
Nʼkuti mulipo ochepa kwambiri komanso muli alendo mʼdzikolo.+
20 Iwo ankayendayenda kuchokera ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,
Komanso kuchokera mu ufumu wina kupita kwa anthu a mtundu wina.+
21 Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awapondereze,+
Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+
22 Iye anati: ‘Musakhudze odzozedwa anga,
Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.’+