-
Yesaya 43:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Usachite mantha chifukwa ine ndili ndi iwe.+
Ndidzabweretsa mbadwa* zako kuchokera kumʼmawa,
Ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kumadzulo.+
6 Ndidzauza kumpoto kuti, ‘Abwezere kwawo!’+
Ndipo ndidzauza kumʼmwera kuti, ‘Usawakanize.
Bweretsa ana anga aamuna kuchokera kutali komanso ana anga aakazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
-