-
2 Samueli 16:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mfumu Davide itafika ku Bahurimu, mwamuna wina wa mʼbanja la Sauli, dzina lake Simeyi,+ mwana wa Gera anatulukira akulankhula mawu onyoza.+ 6 Iye anayamba kugenda Davide, atumiki onse a Mfumu Davide, anthu onse komanso amuna onse amphamvu amene anali kumanja ndi kumanzere kwa mfumu. 7 Simeyi ankanena kuti: “Choka! Choka! Munthu wa mlandu wa magazi ndiponso wopanda pake iwe!
-