-
Mlaliki 2:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Ndinayamba kudana ndi zinthu zonse zimene ndinapeza nditagwira ntchito mwakhama padziko lapansi pano,+ chifukwa ndidzayenera kusiyira munthu amene akubwera pambuyo panga.+ 19 Ndipo ndi ndani akudziwa ngati angadzakhale wanzeru kapena wopusa?+ Koma adzatenga zinthu zanga zonse zimene ndinapeza nditagwira ntchito mwakhama komanso mwanzeru padziko lapansi pano. Zimenezinso nʼzachabechabe.
-
-
Mlaliki 4:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Pali munthu amene ali yekhayekha, wopanda mnzake. Alibe mwana kapena mchimwene wake, koma amangokhalira kugwira ntchito mwakhama. Maso ake sakhutira ndi chuma.+ Koma kodi amadzifunsa kuti, “Ndikamagwira ntchito mwakhama komanso kudzimana zinthu zabwino, kodi ndikufuna kuti zinthu zimenezi adzasangalale nazo ndani?”+ Izinso nʼzachabechabe ndipo ndi ntchito yobweretsa nkhawa.+
-