16 Chifukwa nsembe simukuifuna, mukanakhala kuti mukuifuna ndikanaipereka kwa inu.+
Inu simusangalala ndi nsembe yopsereza yathunthu.+
17 Nsembe zimene Mulungu amasangalala nazo ndi kudzimvera chisoni mumtima.
Inu Mulungu, simudzakana mtima wosweka ndi wophwanyika.+