-
Nyimbo ya Solomo 4:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 “Ndiwe wokongola wokondedwa wanga.
Ndiwe chiphadzuwa.
Maso ako ali ngati maso a njiwa munsalu yako yophimba kumutuyo.
Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi
Zimene zikuthamanga potsika mapiri a ku Giliyadi.+
2 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zomwe angozimeta kumene,
Zimene zikuchokera kosambitsidwa,
Zonse zabereka mapasa,
Ndipo palibe imene ana ake afa.
3 Milomo yako ili ngati chingwe chofiira kwambiri,
Ndipo ukamalankhula umasangalatsa.
Masaya ako munsalu yako yophimba kumutuyo
Ali ngati khangaza* logamphula pakati.
-