-
Deuteronomo 29:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Mʼbadwo wa mʼtsogolo wa ana anu ndiponso mlendo wochokera kudziko lakutali, akadzaona miliri ndi matenda amene Yehova wabweretsa mʼdzikoli—* 23 akadzaona kuti dziko lonse lawonongedwa ndi sulufule, mchere ndi kutentha, moti mʼdzikomo simungadzalidwe mbewu, simungaphuke kalikonse ndipo simungamere chomera chilichonse, ndipo likuoneka ngati Sodomu ndi Gomora,+ Adima ndi Zeboyimu,+ mizinda imene Yehova anaiwononga ndi ukali komanso mkwiyo wake—*
-
-
Yeremiya 25:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Dziko lonseli lidzakhala bwinja ndipo lidzakhala chinthu chochititsa mantha. Mitundu imeneyi idzatumikira mfumu ya ku Babulo zaka 70.”’+
-
-
Yeremiya 45:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Umuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Taona! Zimene ndamanga ndikuzigwetsa ndipo zimene ndadzala ndikuzizula. Ndichita zimenezi mʼdziko lonse.+
-