-
Deuteronomo 11:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Samalani kuti mitima yanu isakopeke nʼkupatuka ndi kuyamba kulambira milungu ina nʼkumaiweramira.+ 17 Mukatero mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo iye adzatseka kumwamba moti mvula sidzagwa+ komanso nthaka sidzapereka zokolola zake. Zikadzatero mudzatha mofulumira mʼdziko labwino limene Yehova akukupatsani.+
-