-
2 Mafumu 16:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Kenako Ahazi anatenga siliva ndi golide wapanyumba ya Yehova ndiponso wochokera mʼnyumba ya mfumu nʼkutumiza kwa mfumu ya Asuri ngati chiphuphu.+ 9 Mfumu ya Asuri inamvera pempho lake ndipo inapita ku Damasiko nʼkukalanda mzindawo. Anthu amumzindawo inawagwira nʼkupita nawo ku Kiri+ ndipo Rezini inamupha.+
-
-
Yesaya 8:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 chifukwa mwanayo asanadziwe kuitana kuti, ‘Ababa!’ kapena ‘Amama!’ chuma cha ku Damasiko ndi katundu wolandidwa ku Samariya zidzatengedwa nʼkupita nazo kwa mfumu ya Asuri.”+
-