-
Yoswa 13:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Kenako Mose anagawira cholowa fuko la Rubeni motsatira mabanja awo. 16 Dera lawo linayambira ku Aroweli, mzinda umene uli mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakatikati pa chigwacho komanso malo onse okwera a Medeba.
-
-
2 Mafumu 10:32, 33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Mʼmasiku amenewo, Yehova anayamba kuchepetsa dziko la Isiraeli pangʼono ndi pangʼono. Ndipo Hazaeli anapitiriza kuukira Aisiraeli mʼmadera awo onse.+ 33 Anayambira kumʼmawa kwa Yorodano, ku Giliyadi konse, dera lonse la Gadi, la Rubeni ndi la Manase,+ kuyambira ku Aroweli yemwe ali pafupi ndi chigwa* cha Arinoni mpaka ku Giliyadi ndi Basana.+
-