-
2 Mafumu 25:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ndiyeno mpanda wa mzindawo unabooledwa+ ndipo asilikali onse anathawa usiku kudzera pageti limene linali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu. Akasidi anali atazungulira mzindawo ndipo mfumu inayamba kuthawa kulowera cha ku Araba.+ 5 Koma asilikali a Akasidi anayamba kuthamangitsa mfumuyo ndipo anaipeza mʼchipululu cha Yeriko. Zitatero asilikali onse a mfumuyo anabalalika nʼkuisiya yokha.
-