-
Yeremiya 4:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Mayo ine,* mayo ine!
Ndikumva kupweteka kwambiri mumtima mwanga.
Mtima wanga ukugunda kwambiri.
-
-
Yeremiya 8:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Chisoni changa nʼchosachiritsika.
Mtima wanga ukudwala.
19 Pakumveka mawu olirira thandizo kuchokera kudziko lakutali,
Kuchokera kwa mwana wamkazi wa anthu anga.
Iye akuti: “Kodi Yehova sali mu Ziyoni?
Kapena kodi mfumu yake mulibe mmenemo?”
“Nʼchifukwa chiyani andikhumudwitsa ndi mafano awo ogoba,
Ndiponso milungu yawo yachilendo yopanda pake?”
-
-
Yeremiya 9:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Ndikanakonda mʼmutu mwanga mukanakhala madzi ambiri,
Ndiponso maso anga akanakhala kasupe wa misozi.+
Zikanatero, ndikanalira masana ndi usiku
Chifukwa cha anthu a mtundu wanga amene aphedwa.
-