-
Yeremiya 5:26-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Chifukwa pakati pa anthu anga pali anthu oipa.
Iwo amabisala nʼkumayangʼanitsitsa ngati mmene amachitira wosaka mbalame.
Amatchera msampha wakupha
Ndipo amagwira anthu.
27 Mofanana ndi chikwere chimene chadzaza mbalame,
Nyumba zawo zadzaza chinyengo.+
Nʼchifukwa chake iwo ali amphamvu komanso alemera kwambiri.
28 Iwo anenepa ndipo asalala.
Akuchita zinthu zoipa zambiri.
-
-
Mika 2:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Tsoka kwa anthu amene amakonza chiwembu,
Amene akagona pabedi pawo, amaganizira kuti achite zoipa.
Ndipo mʼmawa kukacha, amazichitadi.
Chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.+
-
-
Mika 6:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kodi mʼnyumba ya munthu woipa mukupezekabe chuma chopezedwa mopanda chilungamo?
Ndiponso muyezo woperewera wa efa* umene ndi wonyansa?
-