-
2 Mafumu 20:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Pa nthawi imeneyo, Berodaki-baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babulo, anatumiza makalata ndi mphatso kwa Hezekiya chifukwa anamva kuti Hezekiya anadwala.+ 13 Hezekiya analandira anthuwo ndipo anawaonetsa nyumba yake yonse yosungiramo chuma.+ Anawaonetsa siliva, golide, mafuta a basamu, mafuta ena amtengo wapatali, nyumba yake yosungiramo zida zankhondo ndiponso chuma chake chonse. Palibe chimene Hezekiya sanawaonetse mʼnyumba yake* ndi mu ufumu wake wonse.
-