-
2 Mafumu 24:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Nebukadinezara mfumu ya Babulo, anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo atumiki ake atauzungulira.
-
-
2 Mbiri 36:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse, zazikulu ndi zazingʼono, zamʼnyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma cha mʼnyumba ya Yehova, chuma cha mfumu ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse nʼkupita nacho ku Babulo.+
-
-
Danieli 1:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
1 Mʼchaka chachitatu cha ufumu wa Mfumu Yehoyakimu+ ya Yuda, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inabwera ku Yerusalemu ndipo inazungulira mzindawo.+ 2 Kenako Yehova anapereka Mfumu Yehoyakimu ya Yuda mʼmanja mwake,+ limodzi ndi zina mwa ziwiya za mʼnyumba ya* Mulungu woona. Nebukadinezara anatenga ziwiyazo nʼkupita nazo kudziko la Sinara,*+ kunyumba* ya mulungu wake ndipo anakaziika mʼnyumba yosungiramo chuma ya mulungu wake.+
-