-
2 Mafumu 20:16-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ndiyeno Yesaya anauza Hezekiya kuti: “Imva zimene Yehova wanena,+ 17 ‘Masiku akubwera pamene zinthu zonse zimene zili mʼnyumba mwako ndiponso zonse zimene makolo ako akhala akusunga mpaka lero, anthu adzazitenga nʼkupita nazo ku Babulo.+ Palibe chidzatsale,’ watero Yehova. 18 ‘Ena mwa ana ako, amene iweyo udzabereke, adzatengedwa+ ndipo adzakhala nduna zapanyumba ya mfumu ya ku Babulo.’”+
-