-
Deuteronomo 4:34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Kapena kodi Mulungu anayamba wapitapo kukatenga mtundu wa anthu kuti ukhale wake kuchokera pakati pa mtundu wina pogwiritsa ntchito ziweruzo,* zizindikiro, zodabwitsa,+ nkhondo,+ dzanja lamphamvu,+ mkono wotambasula komanso zinthu zoopsa+ zofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Iguputo inu mukuona?
-
-
2 Samueli 7:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Ndi mtundu uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli?+ Inu Mulungu munapita kukawawombola anthu anu+ ndipo munadzipangira dzina+ pamene munawachitira zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha.+ Munathamangitsa mitundu ina ndi milungu yawo chifukwa cha anthu anu amene munawawombola ku Iguputo.
-