-
Yeremiya 33:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena mawu okhudza nyumba zamumzinda uwu ndiponso okhudza nyumba za mafumu a Yuda, zimene zagwetsedwa chifukwa cha malo okwera omenyerapo nkhondo ndiponso lupanga la adani.+
-
-
Ezekieli 4:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 “Iwe mwana wa munthu, tenga njerwa ndipo uiike patsogolo pako. Panjerwapo ujambulepo mzinda wa Yerusalemu. 2 Umenye nkhondo ndi mzindawo+ ndipo umange mpanda womenyerapo nkhondo kuzungulira mzinda wonsewo.+ Umangenso malo okwera omenyerapo nkhondo+ komanso misasa ya asilikali. Uikenso zida zankhondo zogumulira mpanda wa mzindawo kuzungulira mzinda wonsewo.+
-