-
2 Mafumu 25:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Mʼchaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu pamodzi ndi asilikali ake onse.+ Anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo ndipo anamanga msasa komanso mpanda kuzungulira mzinda wonsewo.+ 2 Mzindawo unazunguliridwa mpaka chaka cha 11 cha Mfumu Zedekiya.
-
-
Yeremiya 52:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Mʼchaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara* mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu pamodzi ndi asilikali ake onse. Anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo ndipo anamanga msasa komanso mpanda kuzungulira mzinda wonsewo.+ 5 Mzindawo unazunguliridwa mpaka chaka cha 11 cha Mfumu Zedekiya.
-