-
2 Mbiri 34:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 “Yehova wanena kuti, ‘Ndibweretsa tsoka pamalo ano ndiponso kwa anthu ake,+ pokwaniritsa matemberero onse amene analembedwa mʼbuku+ limene anawerenga pamaso pa mfumu ya Yuda, 25 chifukwa chakuti andisiya+ nʼkumakapereka nsembe zautsi kwa milungu ina kuti andikwiyitse+ ndi ntchito zonse za manja awo, ndibweretsa mkwiyo wanga pamalo ano ndipo suzimitsidwa.’”+
-
-
2 Mbiri 36:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Koma iwo anapitiriza kunyoza atumiki a Mulungu woona,+ kunyoza mawu ake+ ndiponso kuseka aneneri ake.+ Iwo anafika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa. Kenako Yehova anawakwiyira kwambiri nʼkuwalanga.+
17 Choncho anawabweretsera mfumu ya Akasidi+ yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga+ mʼnyumba yopatulika.+ Sinamvere chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena wodwala.+ Mulungu anapereka zonse mʼmanja mwake.+
-