-
Yeremiya 42:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
42 Kenako akuluakulu onse a asilikali, Yohanani+ mwana wa Kareya, Yezaniya mwana wa Hoshaya ndi anthu onse kuyambira anthu wamba mpaka anthu olemekezeka, anapita 2 kwa mneneri Yeremiya nʼkumuuza kuti: “Chonde, tikomere mtima ndipo utipempherere kwa Yehova Mulungu wako. Pempherera anthu onse amene atsalawa chifukwa poyamba tinalipo ambiri koma pano tatsala ochepa+ ngati mmene ukuoneramu.
-