-
Yeremiya 41:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ndiyeno Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali naye anatenga anthu onse amene anatsala ku Mizipa. Anthu amenewa ndi amene anawapulumutsa mʼmanja mwa Isimaeli mwana wa Netaniya amene anawagwira atapha Gedaliya+ mwana wa Ahikamu. Anapulumutsa amuna, asilikali, akazi, ana ndi nduna zapanyumba ya mfumu ndipo anabwera nawo kuchokera ku Gibiyoni.
-
-
Yeremiya 42:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
42 Kenako akuluakulu onse a asilikali, Yohanani+ mwana wa Kareya, Yezaniya mwana wa Hoshaya ndi anthu onse kuyambira anthu wamba mpaka anthu olemekezeka, anapita 2 kwa mneneri Yeremiya nʼkumuuza kuti: “Chonde, tikomere mtima ndipo utipempherere kwa Yehova Mulungu wako. Pempherera anthu onse amene atsalawa chifukwa poyamba tinalipo ambiri koma pano tatsala ochepa+ ngati mmene ukuoneramu. 3 Yehova Mulungu wako atiuze njira yoti tiyendemo ndi zoti tichite.”
-