-
2 Mbiri 36:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwachenjeza kudzera mwa atumiki ake. Ankawachenjeza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo ndiponso malo ake okhala. 16 Koma iwo anapitiriza kunyoza atumiki a Mulungu woona,+ kunyoza mawu ake+ ndiponso kuseka aneneri ake.+ Iwo anafika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa. Kenako Yehova anawakwiyira kwambiri nʼkuwalanga.+
-
-
Yesaya 65:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu amakani,+
Kwa anthu amene akuyenda mʼnjira yoipa,+
Potsatira maganizo awo,+
-
Yeremiya 7:24-26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu.+ Mʼmalomwake, anayenda motsatira zofuna zawo. Mouma khosi anatsatira zofuna za mtima wawo woipawo,+ moti anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo, 25 kuchokera tsiku limene makolo anu anatuluka mʼdziko la Iguputo mpaka pano.+ Choncho ndinapitiriza kukutumizirani atumiki anga onse omwe ndi aneneri, ndinkawatumiza tsiku lililonse, mobwerezabwereza.*+ 26 Koma iwo anakana kundimvera ndipo sanatchere khutu lawo.+ Mʼmalomwake anaumitsa khosi lawo ndipo ankachita zinthu zoipa kuposa makolo awo.
-
-
Yeremiya 35:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndinkakutumizirani mobwerezabwereza*+ atumiki anga onse omwe anali aneneri. Ndinkawauza uthenga wakuti, ‘Chonde bwererani ndipo aliyense asiye njira zake zoipa.+ Muzichita zinthu zabwino. Musatsatire milungu ina nʼkumaitumikira. Mukatero mudzapitiriza kukhala mʼdziko limene ndinapatsa inuyo ndi makolo anu.’+ Koma inu simunatchere khutu kapena kundimvera.
-
-
-