-
Yesaya 15:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
Nʼchifukwa chake amuna onyamula zida a ku Mowabu akungofuula.
Iwo akunjenjemera kwambiri.
5 Mtima wanga ukulirira Mowabu.
Anthu ake athawira kutali, ku Zowari+ ndi ku Egilati-selisiya.+
Iwo akulira pamene akukwera mtunda wa Luhiti.
Panjira yopita ku Horonaimu, iwo akulira kwambiri chifukwa cha tsokalo.+
6 Madzi a ku Nimurimu aumiratu.
Msipu wobiriwira wauma,
Udzu watha ndipo palibenso chilichonse chobiriwira chimene chatsala.
-