-
Obadiya 2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Taona! Ndakuchititsa kukhala wosafunika pakati pa mitundu ina,
Ndipo ikukuona kuti ndiwe wonyozeka kwambiri.+
3 Mtima wako wodzikuza wakupusitsa,+
Iwe amene ukukhala mʼmalo obisika amʼthanthwe,
Uli pamwamba pa phiri nʼkumanena mumtima mwako kuti,
‘Ndani angandigwetsere pansi?’
4 Ngakhale utamakhala mʼmwamba* ngati chiwombankhanga,
Kapena utamanga chisa chako pakati pa nyenyezi,
Ine ndidzakugwetsapo pamenepo,” akutero Yehova.
-