-
Yesaya 34:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Yehova ali ndi lupanga. Lupangalo lidzakhala magazi okhaokha.
Lidzakhala mafuta okhaokha,+
Lidzakhala ndi magazi a nkhosa zamphongo zingʼonozingʼono komanso a mbuzi,
Lidzakhala ndi mafuta a impso za nkhosa zamphongo.
Chifukwa Yehova adzapereka nsembe ku Bozira,
Adzapha nyama zambiri mʼdziko la Edomu.+
-
-
Yesaya 34:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Usiku kapena masana motowo sudzazimitsidwa.
Utsi wake udzapitiriza kukwera mʼmwamba mpaka kalekale.
Dzikolo lidzakhala lowonongedwa ku mibadwomibadwo.
Mpaka muyaya, palibe amene adzadutsemo.+
-