-
Yesaya 34:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Yehova ali ndi lupanga. Lupangalo lidzakhala magazi okhaokha.
Lidzakhala mafuta okhaokha,+
Lidzakhala ndi magazi a nkhosa zamphongo zingʼonozingʼono komanso a mbuzi,
Lidzakhala ndi mafuta a impso za nkhosa zamphongo.
Chifukwa Yehova adzapereka nsembe ku Bozira,
Adzapha nyama zambiri mʼdziko la Edomu.+
7 Ngʼombe zamphongo zamʼtchire zidzapita nawo limodzi,
Ngʼombe zingʼonozingʼono zamphongo zidzapita limodzi ndi zamphamvu.
Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha,
Ndipo fumbi lamʼdziko lawo lidzanona ndi mafuta.”
-
-
Ezekieli 39:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Mudzadya mnofu wa anthu amphamvu komanso kumwa magazi a atsogoleri a dziko lapansi, omwe ndi nkhosa zamphongo, ana a nkhosa amphongo, mbuzi ndi ngʼombe zamphongo, nyama zonse zonenepa za ku Basana.
-