19 Amoni+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 22 ndipo analamulira zaka ziwiri ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Yotiba ndipo dzina lawo linali Mesulemeti mwana wa Haruzi. 20 Amoni ankachita zoipa pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Manase bambo ake.+