-
Danieli 1:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
1 Mʼchaka chachitatu cha ufumu wa Mfumu Yehoyakimu+ ya Yuda, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inabwera ku Yerusalemu ndipo inazungulira mzindawo.+ 2 Kenako Yehova anapereka Mfumu Yehoyakimu ya Yuda mʼmanja mwake,+ limodzi ndi zina mwa ziwiya za mʼnyumba ya* Mulungu woona. Nebukadinezara anatenga ziwiyazo nʼkupita nazo kudziko la Sinara,*+ kunyumba* ya mulungu wake ndipo anakaziika mʼnyumba yosungiramo chuma ya mulungu wake.+
-