18 “Mika+ wa ku Moreseti nayenso ankanenera mʼmasiku a Mfumu Hezekiya+ ya ku Yuda. Iye ankauza anthu onse a ku Yuda kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:
“Ziyoni adzalimidwa ngati munda,
Yerusalemu adzakhala mabwinja,+
Ndipo phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda zamunkhalango.”’+