-
2 Mafumu 17:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti Aisiraeli anachimwira Yehova Mulungu wawo, yemwe anawatulutsa mʼdziko la Iguputo nʼkuwachotsa mʼmanja mwa Farao mfumu ya Iguputo+ ndipo anayamba kulambira* milungu ina.+ 8 Iwo ankatsatira miyambo ya mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa Aisiraeli ndiponso ankatsatira miyambo imene mafumu a Isiraeli anayambitsa.
-