Miyambo
31 Mawu a Mfumu Lemueli, uwu ndi uthenga wamphamvu umene mayi ake anamupatsa pomulangiza:+
2 Kodi ndikuuze chiyani mwana wanga?
Kodi ndikuuze mawu otani iwe mwana wochokera mʼmimba mwanga?
Kodi ndikuuze mawu otani iwe mwana wa malonjezo anga?+
3 Usamapereke mphamvu zako kwa akazi,+
Kapena kutsatira njira zimene zimachititsa kuti mafumu awonongedwe.+
4 Nʼkosayenera kuti mafumu azimwa vinyo,
Nʼkosayenera kuti mafumu azichita zimenezi, iwe Lemueli,
Kapena kuti olamulira azinena kuti: “Kodi chakumwa changa chili kuti?”+
5 Chifukwa angamwe nʼkuiwala malamulo
Ndiponso kupondereza ufulu wa anthu onyozeka.
7 Asiyeni amwe kuti aiwale umphawi wawo,
Ndipo asakumbukirenso mavuto awo.
8 Lankhula poteteza anthu amene sangathe kudziteteza okha.
Teteza ufulu wa anthu onse amene akuwonongedwa.+
א [Aleph]
10 Kodi ndi ndani amene angapeze mkazi wamakhalidwe abwino?*+
Ndi wamtengo wapatali kuposa miyala ya korali.*
ב [Beth]
11 Mwamuna wake amamudalira ndi mtima wonse,
Ndipo mwamunayo amapeza chilichonse chimene akufunikira.
ג [Gimel]
12 Masiku onse a moyo wake,
Mkaziyo amachitira mwamuna wakeyo zinthu zabwino osati zoipa.
ד [Daleth]
13 Amatenga ulusi ndi nsalu,
Ndipo amasangalala kugwira ntchito ndi manja ake.+
ה [He]
14 Iye ali ngati sitima zapamadzi za munthu wamalonda,+
Amabweretsa chakudya chake kuchokera kutali.
ו [Waw]
15 Amadzukanso kudakali usiku,
Nʼkupereka chakudya kwa banja lake
Ndipo atsikana ake antchito amawapatsa gawo lawo.+
ז [Zayin]
16 Amaganizira zogula munda ndipo amauguladi.
Amalima munda wa mpesa chifukwa cha khama lake.*
ח [Heth]
ט [Teth]
18 Amaonetsetsa kuti akupeza phindu pa malonda ake.
Nyale yake simazima usiku.
י [Yod]
19 Manja ake amagwira ndodo yokulungako ulusi,
Ndipo zala zake zimagwira ndodo yopotera chingwe.+
כ [Kaph]
20 Amatambasula dzanja lake nʼkuthandiza munthu wonyozeka,
Ndipo amatambasula manja ake kuti athandize wosauka.+
ל [Lamed]
21 Kukamazizira, iye sadera nkhawa za banja lake
Chifukwa anthu onse a mʼbanja lake amavala zovala zotentha.*
מ [Mem]
22 Iye amapanga yekha zoyala pabedi.
Zovala zake zimakhala za nsalu zabwino ndiponso za ubweya wa nkhosa wapepo.
נ [Nun]
23 Mwamuna wake amadziwika bwino pamageti a mzinda,+
Pamene amakhala pamodzi ndi akulu amʼdzikolo.
ס [Samekh]
24 Iye amapanga zovala* nʼkuzigulitsa,
Ndipo amapanga malamba nʼkuwapereka kwa amalonda.
ע [Ayin]
25 Iye amavala mphamvu ndi ulemerero ngati chovala,
Ndipo sada nkhawa akamaganizira zamʼtsogolo.
פ [Pe]
צ [Tsade]
27 Iye amayangʼanira ntchito zapabanja pake,
Ndipo sadya chakudya cha ulesi.+
ק [Qoph]
28 Ana ake amaimirira nʼkumutchula kuti ndi wosangalala.
Mwamuna wake amaimirira nʼkumutamanda kuti:
ר [Resh]
29 “Pali akazi ambiri amakhalidwe abwino,*
Koma iweyo umaposa onsewo.”
ש [Shin]
30 Munthu akhoza kuoneka ngati wabwino koma zisali choncho ndipo kukongola sikungachedwe kutha,*+
Koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.+
ת [Taw]