Miyambo
6 Mwana wanga, ngati walonjeza kuti udzapereka ngongole ya mnzako iye akadzalephera kubweza,+
Ngati wagwirana dzanja ndi mlendo pochita mgwirizano,+
2 Ngati wakodwa ndi lonjezo limene unapanga,
Ngati wagwidwa ndi mawu amʼkamwa mwako,+
3 Uchite izi mwana wanga kuti udzipulumutse,
Chifukwa uli mʼmanja mwa mnzako:
Pita ukadzichepetse ndipo ukamuchonderere kwambiri mnzakoyo.+
4 Usalole kuti maso ako agone,
Kapena kuti zikope zako ziwodzere.
5 Dzipulumutse ngati insa mʼmanja mwa wosaka,
Ndiponso ngati mbalame mʼmanja mwa wosaka mbalame.
6 Pita kwa nyerere waulesi iwe,+
Ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru.
7 Ngakhale kuti ilibe mtsogoleri, kapitawo, kapena wolamulira,
8 Imakonza chakudya chake mʼchilimwe,+
Ndipo imasonkhanitsa chakudya chake pa nthawi yokolola.
9 Kodi waulesi iwe, ugona pamenepo mpaka liti?
Kodi udzuka nthawi yanji kutulo tako?
10 Ukapitiriza kugona pangʼono, ukapitiriza katulo pangʼono,
Ukapitiriza kupinda manja pangʼono kuti upume,+
11 Umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba,
Ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+
12 Munthu wopanda pake komanso woipa, amangoyendayenda nʼkumalankhula mabodza.+
13 Amatsinzinira ena diso lake,+ amachita zizindikiro ndi phazi lake ndiponso amachita zizindikiro ndi zala zake.
14 Popeza mtima wake ndi wachinyengo,
Nthawi zonse amakonza ziwembu+ komanso amakhalira kuyambanitsa anthu.+
15 Choncho tsoka lake lidzabwera mwadzidzidzi.
Adzathyoledwa modzidzimutsa moti sadzachira.+
16 Pali zinthu 6 zimene Yehova amadana nazo.
Zilipo zinthu 7 zimene amanyansidwa nazo:
17 Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja amene amakhetsa magazi a anthu osalakwa,+
18 Mtima umene umakonza ziwembu,+ mapazi othamangira kukachita zoipa,
19 Mboni yachinyengo imene nthawi zonse imanena mabodza,+
Komanso aliyense amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.+
21 Uwamange pamtima pako nthawi zonse
Ndipo uwamange mʼkhosi mwako.
23 Chifukwa lamulolo ndi nyale,+
Ndipo malangizo ndi kuwala,+
Komanso kudzudzula kumene kumathandiza munthu kusintha ndi njira yakumoyo.+
25 Usasirire kukongola kwake mumtima mwako.+
Kapena kulola kuti ukopeke ndi maso ake achikoka,
26 Munthu amafika potsala ndi mkate umodzi wokha chifukwa cha hule,+
Koma mkazi wa mwini amasaka moyo wako wamtengo wapatali.
27 Kodi munthu anganyamule makala a moto pachifuwa pake, zovala zake osapsa?+
28 Kapena kodi munthu angayende pamakala a moto, mapazi ake osapsa?
29 Nʼchimodzimodzi ndi aliyense wogona ndi mkazi wa mnzake.
Aliyense wokhudza mkaziyo adzalangidwa.+
30 Anthu sanyoza munthu wakuba
Ngati waba kuti apeze chakudya pamene ali ndi njala.
31 Koma akapezeka, adzabweza zinthuzo kuwirikiza ka 7.
Adzapereka zinthu zonse zamtengo wapatali zamʼnyumba mwake.+
32 Aliyense wochita chigololo ndi mkazi ndi wopanda nzeru.*
Amene amachita zimenezi amadzibweretsera mavuto aakulu pa moyo wake.+
34 Chifukwa nsanje imachititsa kuti mwamuna wake akwiye kwambiri.
Pomubwezera sadzamva chisoni.+
35 Iye sadzavomera chipukuta misozi chilichonse,*
Ndipo sadzapepeseka ngakhale utapereka mphatso yaikulu bwanji.