Salimo
Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide.
133 Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri
Abale akakhala pamodzi mogwirizana!+
2 Zili ngati mafuta abwino amene athiridwa pamutu+
Amene akuyenderera pandevu,
Ndevu za Aroni,+
Ndipo akuyenderera mpaka mʼkolala ya zovala zake.
Kumeneko nʼkumene Yehova analonjeza kuti kudzakhala madalitso ake,
Omwe ndi moyo wosatha.